Moses Chikolosa Dekha Official Video

D-E-K-H-A is a song aimed at giving hope to the hopeless.
“The Lord is always good. He is always loving and kind, and his faithfulness goes on and on to each succeeding generation.”
Psalm 100:5
Mkutheka mwakulira banja la Chikhristu- mwaphunzira kukhala mmoyo wa pemphero nthawi zonse;
Mwakhala mukupempherela chakudya chilichonse-
Mwakhala mukupemphela pogona komanso podzuka-
Mwakhala mukupempherela chilichonse kaya chichepe bwanji!
Muzonsezi, phunziro lalikuli linali lakuti Mulungu ndiwabwino.
Funso mkumati Kodi Mulungu ndiwabwinodi?
Mulungu ndiwabwino pamene inu mwanamiziridwa?
Mulungu ndiwabwino pamene Okondedwa wanu wakusiyani?
Kodi Mulungu ndiwabwinobe pamene ntchito akuchotsani?
Kodi Mulungu ndiwabwino pamene ngakhale kuyesetsa kwanu kotani koma zinthu sizikusintha?
Moyowu munthu ungapitirize bwanji kukhulupilirabe Mulungu muzinthu zotopetsa?
Abale dziwani izi:
Pamene tikukumana ndi nyengo zowawa zimaoneka ngati mawa silifika komanso ngati kuti oyamba kukumana ndi zoterozo ndi ifeyo.
Ineyo personally ndadutsanso munyengo zowawa zimene pena kumadziona ngati ukamaliza kulota udzuka koma ayi ndithu ulimoyo weniweni.
1. Ndanamiziridwapo mpakana ku Chichiri Prison
2. Kugula chinthu chodula kungotha mwezi umodzi Katundu kukubela chonsecho munthu unali ku mapemphero.
3. Kugula galimoto in a space of 1 month kuchita ngozi yochititsa mantha.
4. Kulembedwa ntchito ndikupanga ma plan a moyo koma mukanthawi kochepa kuchotsedwanso.
5. Kukanidwa kupatsidwa mwayi pa zinthu zingapo akuti chifukwa umaoneka opemphera kwambiri......
6. Kuchedwetsedwa mu zopemphera zina zoswetsa mtima m'moyo.
Ndikudziwa kuti nanunso mwadutsa komanso mukudutsa muzinthu zowawa. Dziwani kuti nyengo zathu sizipanga define Mulungu.
Mulungu ali chimene ali chifukwa Cha chimene ali.
Limbikitsikani kuti Mulungu sanakusiyeni ndipo ali nanu.
Limbikitsikani kuti Mulungu amasamala.
Limbikitsikani kuti Mulungu amabweseretsa.
Limbikitsikani kuti Mulungu akudziwa.
Limbikitsikani kuti Mulungu amamvetsera.
Limbikitsikani kuti amaona.
Inuyo DEKHANI.
Dziko lapansi akulamulira ndi Mulungu, ndipo timetable yake ndi yosiyana ndi imene ife timagwiritsa ntchito nthawi zambiri.
Khazikikani pa chikondi Cha Mulungu osati zomwe moyo wanu ukudutsa kapena zimene mumafuna mutakwaniritsa.
Mukaonetsetsa, mudzapeza kuti Pali anthu ena ali pansi komanso pamwamba pa moyo wanu.
Inuyo Dekhani.
Zoonadi kuti Chaka chikutha ndipo maloto aja sanatheke koma inuyo DEKHANI.
Anthu ambiri amene anadikirira pa Mulungu anayankhidwa modabwitsa:
1. Hannah anapatsidwa Samuel-
2. Sarah anapatsidwa Isaac-
3. Elizabeth anapatsidwa John the Baptist-
4. Martha anaona brother wake atauka Kwa akufa-
5. Simon anaona Mpulumutsi-
6. Noah anatsegulilidwa mungalawa-
7. Rehab anapulumutsidwa ndi banja lake lonse.
8. Joseph anatsogozedwa ndi Mulungu ndipo maloto okhala otsogolera anathekera ku dziko lachilendo.
9. David anakhala Mfumu koma atadzozedwa kokwana katatu.
Inuyo DEKHANI.

Пікірлер